MA BANKER AMWA WAMKAKA

21 Aug 2026

Timu ya Silver strikers yayamba bwino ulenso wake mu mpikisano wa CAF pamene yapambadza Costol Do Sol ya mdziko la Mozambique 2:1 lachisanu pa 21 August 2026. lachisanu pa 21 August 2026. Ma banker ameneanayamba mkutsalira. Mmasewerowa, anachokera kumbuyo ndikugonjetsa atsika aku Moshikowa kuchititsa kuti Ma banker abwelere kuno kumudzi akumwemwetera. Ireen Khumalo yemwenso ndi mmodzi mwa osewera amene achita bwino ku WAFCON ndi timu ya Scorchers, anasankhidwa ngati amene anasewera bwino mmasewerowa. Khumalo wasiya mbiri pamenenso anamwetsa chigoli chapamwamba chopambanira kudzera pa free kick. Silver Strikers ili mu gulu B limodzinso ndi matimu a Mamelodi Sundowns oyaku South Africa komanso Nsingizini Hotspurs yaku Eswatini.

← Back to News