TIKUKUFUNIRANI ULENDO WABWINO ACHINYAMATA NONSE

26 Aug 2026

Komiti yaikulu ya achinyamata a mpingo wa Churches of Christ, Gowa Synod yati ikufunira achinyamata onse ulendo wabwino pamene akhale akulowera ku Malonda lachitatu pa 26 August 2026. Mu kalata imene yasainidwa ndi mkhala pampando Stanley Mpaha komanso mlembi wamkulu Helbert Chakwawa, yati atsogoleriwa akufunira achinyamata onse amene akhale akulowera ku Malonda primary school kumene akhale ndi msonkhano wawo wa pachaka ulendo opanda zophunthwitsa malinga ndi Masalimo 121 vesi 7 ndi 8. Msonkhanowu omwe waitanitsa achinyamata a mpingowu mmadera onse, uchitika pa mutu oti *'' Tikhale Woyera pakuti Yehova ndi Woyera''* kuchokera pa 1 Petr 1 vesi 16. Magulu oimba monga New Salvation kuchokera ku Lilongwe, Kaludzu yaku Ntcheu komanso Galilee yaku Blantyre ndi ena mwa makwaya ochuluka amene akakhale akutumikira mmaimbidwe mothandizana ndi Mlaliki Nestah komanso uja wa kumaliopa mawa Alex Nkalo. Ena mwa okatumikira ku msonkhanowu ndi a Moderator a Synod ya Gowa m' busa Harden Chitseko, wachiriwi kwa mlembi wamkulu m'busa Queen Phiri komanso m'busa Yasin Gama kuchokera ku Mvama CCAP. Msonkhano wapachakawu ukachitikira pabwalo la zamasewero la Malonda Primary School ndipo uyamba lachitatu pa 26 mpaka LaMulungu pa 30 August 2026. By Goodwin Chidoola

← Back to News