26 Aug 2026
Katswiri oyimba wa dziko la America odziwika ndi luso lapamwamba komanso timawu tanthetemwa, Dolly Parton wamwalira lachiwiri pa 26 August chaka chino. Parton ndi oyimba wa zaka zammbuyomo, yemwe adachititsa moyo wachikondi kwa makolo athu mmbuyomu kukhala ozuna. Kamba ka luso lake, mayiyu adapambana mphoto za Grammy khumi komanso adalemba nyimbo zoposa 3000. Parton wamwalira ali ndi zaka makumi asanu ndi atatu (80) atadwala kwa nthawi ndipo mmbuyomu wakhala akuvutika ndi ipso komanso mtima. Rest in peace Legend : By Goodwin Chidoola
← Back to News