PARLIAMENT IFUFUZA MPUNGWEPUNGWE KU BT WATER BOARD

02 Sep 2026

Sipikala wanyumba ya malamulo Sameer Suleiman wati makomiti ake apadera fufuza za kusamvana komwe kulipo ku bungwe logawa madzi la Blantyre Water Board, BWB. Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani lachitatu pa 2 September chaka chino, Suleiman wati nyumba ya malamulo yalandira madandaulo kuchokera ku bungwe logawa madzi'li ndipo ati achita kanthu. '' Madandaulo ena abwera ndi ma umboni kuti ena akumaonetsa ngati makampani agwira ntchito ndikudzilipira okha zomwe sizinachitike. '' Poonjezera apa, Suleiman wati pali mphekesera kuti thandizo la ndalama zogulira ma mita zomwe zikubwera ndi zomwe zikuganiziridwa kuti zikubweretsa kusamvanaku. Mkulu wa bungweli wakhakala akuimitsidwa pa udindowu kawiri konse ndipo bwalo la milandu ndilo lakhala likumubwenzeretsa. Tidziti parliament yayambadi kudziimira payokha? : Goodwin Chidoola

← Back to News